23:1Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
2Amandigoneka pa msipu wobiriwira,
amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
3amatsitsimutsa moyo wanga.
Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo
chifukwa cha dzina lake.
4Ngakhale ndiyende
mʼchigwa cha mdima wakuda bii,
sindidzaopa choyipa,
pakuti Inu muli ndi ine;
chibonga chanu ndi ndodo yanu
zimanditonthoza.
5Mumandikonzera chakudya
adani anga akuona.
Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta;
chikho changa chimasefukira.
6Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata
masiku onse a moyo wanga,
ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova
kwamuyaya.
KUFOTOKOZERA
Kufunsa aliyense afotokozere m'mene wamvera mawuwo
ZOYENERA KULINGALIRA
- Kodi mawu awa akundiphunzitsa chiyani za Mulungu?
- Kodi mawu awa akundiphunzitsa chiyani za anthu?
- Ngati mawu a Mulungu akulankhula ndi moyo wanga, ndidzanvera motani?
- Kodi ndikadziwitsa yani?
Get Discovery Bible Studies on your phone
Discover copyright ©2015-2026 discoverapp.org
Chichewa scriptures from Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™. Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. All rights reserved